Times 360 Malawi, Jan 6 #Times360Malawi Mtsogoleri wa chipani cha People's Transformation (Petra) a Kamuzu Chibambo wati ndi zokhumudwitsa kuti malonjezo ambiri a mgwirizano wa Tonse kwa Amalawi sakukwaniritsidwa. A Chibambo atinso kugwa kwa ndalama ya Kwacha ndi malinga ndi zisankho zosakhala bwino zimene atsogoleri a dziko lino akhala akupanga. Iwo ati chipani chawo chabwera kudzalimbana ndi umphawi umene ukuzunza Amalawi chifukwa akudziwa kuti ndi zotheka dziko lino kuchoka mu umphawiwu. A Chibambo akuyankhula izi mu mzinda wa Blantyre pamene chipani chawo chikukhazikitsa tsamba la pa intaneti (website). Chipani cha Petra chidali nawo mu mgwirizano wa Tonse koma chidalengeza kuti chatuluka.